Makoponi afika ku Kasungu
Kuli chimwemwe kwa alimi pafupifupi 50,000 m’boma la Kasungu pomwe makoponi pansi pa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya Farm Inputs Subsidy Program (FISP), afika tsopano. Boma la Kasungu lalandira makoponi omwe alimi okwana 48,596 omwe adalembetsedwa agwiritse ntchito pogulira feteleza mu ndondomeko ya FISP.A Loveness Kapachika omwe anayimira bwanamkubwa wabomali a Lawford...
uli chimwemwe kwa alimi pafupifupi 50,000 m’boma la Kasungu pomwe makoponi pansi pa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya Farm Inputs Subsidy Program (FISP), afika tsopano.
Boma la Kasungu lalandira makoponi omwe alimi okwana 48,596 omwe adalembetsedwa agwiritse ntchito pogulira feteleza mu ndondomeko ya FISP.
A Loveness Kapachika omwe anayimira bwanamkubwa wabomali a Lawford Palani pa mwambo olandira makoponiwa, anati iwo ndi okondwa chifukwa choti makoponiwa abwera munthawi yabwino.
A Kapachika ati ali ndi chikhulupiliro kuti fetereza abweranso munthawi yabwino zomwe zithandizire kuti alimi alime munthawi yabwino.
Iwo anati bomali layika kale ndondomeko zoti makoponiwa apite kwa alimi msanga ndipo atsimikiza kuti ntchitoyi iyamba kuchokera Lolemba lino.
Apa a Kapachika apempha alimi omwe alandire nawo makoponiwa kuti asagulitse ndicholinga choti zidzawapindulire pa mawa.
Poyankhulapo, mkulu wa apolisi m’bomali a Alexander Moyo ati ngati apolisi awonetsetsa kuti pali chitetezo chokwanira kufikira atalandira makoponiwa.
Alimi akuyembekezeka kulandira makoponiwa kudzera m’magulu ndipo adzagwilitsa ntchito koponiyi pogulira feteleza wanthaka ndi obereketsa.
Alimiwa adzagwilitsa ntchito feteleza-yu popangira feteleza wa Mbeya omwe adzagawane matumba 5 a mbeya obereketsa komanso ena 5 okulitsa pa banja lililonse kuti adzathire m’munda wawo okwana ekala imodzi.
Makoponiwa aperekedwa kudzera m’magulu a alimi okwana 320 omwe ali m’zigawo zonse za ulimi (EPA) zokwana khumi (10) zomwe zili m’bomali.
Did you enjoy this article?
Recommend it — Standard Reader surfaces well-loved writing to more readers across the network.